20/03/2025
Kodi timanva bwanji pa imfa ya Yesu?
Ndizonvesa chisoni kwambili kuti nkhanza padzikoli zinayamba kalekale kufikila pano nkhaza zikupitililabe ndikutelo chifukwa tikawona ndimomwe dzikoli lili pano ariyese akadzuka ndi moyo kwatsiku limenelo akuyamika kumwamba 🙏
Yesu anazunzidwa momamukwapula zomwe zinali zopanda wulemu mpaka kumukoloweka chthu cholemela kuti aziyenda nacho kwinaku akukwapulidwa abale ndi imfa yowawa kuvulidwa zovala nkumakwapulidwa kumangidwa manja ndi zigwe zomwe zinali nkhaza kwaiyeyu
Zinalizovuta kuti iye athawe chifukwa anali kukhulupilila mulungu komanso zinali zolembedwa kale kuti adzapangidwa chipogwe padzikoli NDE nkhaza zimenezi panoso zilipo ndipo zilidzokolonse lapasi timatchula dzina la Yesu chifukwa iye anasonyeza kulimba mtima kunali kumuukila ndipodi athuwo anapangadi kufuna kwawo Yesu analimba mtima povomeleza pachimenechi
Zinalizonvesa chisoni kupachikidwa pantanda Mai ake akuwona (maria) ndipo anakhomedwa ali wamoyopantanda iye aliponpo anayankhula mawu omwe lelolino ndi chipulumutso cha athu a dziko lonse lapansi ndani mwaife angakhomedwe misomali nmanja onse awili mowatambasula kuphatikizapo miyendo koma nkukhalabe ndimoyo komanso nphanvu kukwanitsa kuyankhula? Ndani mwaife angalole kupeleka moyo wake kwamitumduyonse pofuna kubweletsa ntendele? Ndikukhulupilila sangapezeke yesu anapanga zonsezi yekha ndipo lelo ndichifukwa chake tikutansa ndi mawufulu oti wina anatikonzela kale
Tikuyenera kukhala achifundo nthawizonse powafunila azathu zabwino kapena kugwananawo zithu zomwe tilinanzo Yesu anasonyeza kulimba mtima mwachikhulupilo ndipodi athu analitu kulikita ngati simuthu nzawo ai samalemekezaso ai kodi pano sitimalemekeza atsongolele amaiko or anpingo? Timawalemekeza chifukwa ndi opatulika koma wufulu osewu anamenya ndi yesu podzipeleka yekha ku imfa
Awuzeni anebawo kuti ndinu opatulika chifukwa yesu anakufelani wufumu omwe mulinawowu anakumenyelani ndi Yesu kwaine ndimaphuzila zambili komanso ndimakhulupilila